Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:40 - Buku Lopatulika

40 Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Tsono adapakula naŵapatsa anthuwo kuti adye. Koma pamene adayamba kudya chakudyacho, anthuwo adafuula kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, muli dziphe m'nkhalimu.” Choncho sadathe kudya chakudyacho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:40
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka:


Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?


Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.


Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.


Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba paphiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.


Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m'funga mwake, nadza, nazichekerachekera m'nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe.


Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wake, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano chipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu.


Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha.


Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara.


adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.


Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israele asanafe, ndi uwu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa