Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:26 - Buku Lopatulika

26 uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Thamanga msanga ukamchingamire, ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi nkwabwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Nanga mwana uja ali bwino?’ ” Mkaziyo adayankha Gehazi kuti, “Inde, nkwabwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’ ” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:26
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.


Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.


Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?


Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.


Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.


Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;


Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.


Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri.


Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao.


Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa