Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:25 - Buku Lopatulika

25 Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Motero adayenda nakafika kwa Elisa, munthu wa Mulungu uja, ku phiri la Karimele. Tsono mneneri Elisa ataona kuti mai uja akudza, adauza Gehazi mtumiki wake kuti, “Taona patsidyapo, Msunamu uja akubwera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo!

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:25
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.


Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.


Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba paphiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.


Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.


Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.


uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.


Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.


Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.


Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita.


Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa