Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Apo mwamuna wakeyo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukupita kwa iyeyo lero? Lerotu si tsiku lokhala mwezi, kapenanso tsiku la Sabata ai.” Mai uja adati, “Palibe kanthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:23
9 Mawu Ofanana  

Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.


Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.


ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova;


Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;


Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;


Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa