Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:14 - Buku Lopatulika

14 Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndipo Elisa adafunsanso Gehazi kuti, “Nanga tsono timchitire chiyani?” Gehazi adayankha kuti, “Pepani, mai ameneyu alibe mwana wamwamuna, ndipo mwamuna wake ngwokalamba.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Elisa anafunsanso Gehazi kuti, “Kodi tingamuchitire chiyani?” Gehazi anati, “Ndithu, mayiyu alibe mwana ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:14
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?


Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.


Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.


Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.


Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.


Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.


Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.


Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.


Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa