2 Mafumu 4:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Elisa adalamula Gehazi kuti amuuze maiyo kuti, “Ndithu mwavutika potichitira zonsezi. Nanga ife tikuchitireni chiyani? Kodi muli ndi mau oti tikakunenereni kwa mfumu, kapena kwa mtsogoleri wankhondo?” Maiyo adayankha kuti, “Ine ndimakhala mwaufulu pakati pa anthu a mtundu wanga.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’ ” Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.” Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.