Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:10 - Buku Lopatulika

10 Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikaponyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tiyeni timmangire kachipinda kakang'ono kam'mwamba, ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi nyale, kuti nthaŵi zonse akatichezera, azitha kumakakhala m'menemo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tiyeni timumangire kachipinda kakangʼono pa denga la nyumbayi ndi kumuyikiramo bedi ndi tebulo, mpando ndi nyale. Akabwera kuno azikhala mʼmenemo.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.


Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'chipinda chosanja, nagona komweko.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.


ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa