Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo ataona mfumu ya Mowabu kuti nkhondo idamuvuta, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo ataona mfumu ya Mowabu kuti nkhondo idamlaka, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Mfumu ya Amowabu itaona kuti nkhondo yaŵaipira, idatenga anthu 700 amalupanga, kuti athaŵe modutsa ankhondo kupita kwa mfumu ya ku Edomu, koma adalephera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:26
5 Mawu Ofanana  

Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.


Pamenepo anagwira mwana wake wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwake, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israele kwambiri; potero anamchokera, nabwerera ku dziko lao.


Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.


Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa