2 Mafumu 3:25 - Buku Lopatulika25 Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Napasula midzi, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake m'Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Tsono Aisraele adagumula mizinda yao, ndipo pa munda uliwonse wachonde aliyense ankaponyapo mwala, mpaka minda yonse idadzaza ndi miyala. Adatseka akasupe onse, nagwetsa mitengo yonse yabwino. Kudatsala mzinda wa Kiri-Haresefi wokha, koma pambuyo pake ankhondo oponya miyala adabwera naugonjetsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo. Onani mutuwo |