Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:21 - Buku Lopatulika

21 Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'chuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'chuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono Amowabu atamva kuti mafumu atatu abwera kuti achite nawo nkhondo, adaitana onse amene ankatha kumenya nkhondo kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Onsewo adakandanda ku malire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:21
4 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.


Ndipo kunachitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.


Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amowabu madzi ali pandunji pao ali psu ngati mwazi;


Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa