Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo kunachitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo kunachitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 M'maŵa mwake, nthaŵi yopereka nsembe ili pafupi, adangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, mpaka malowo adadzaza madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:20
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.


Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'chuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.


Asanduliza chipululu chikhale thawale, ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.


Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako ndi mitsinje inasefuka; kodi adzakhozanso kupatsa mkate? Kodi adzafunira anthu ake nyama?


inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa