Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo mudzakantha mizinda yonse ya malinga, ndi mizinda yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo mudzakantha midzi yonse ya malinga, ndi midzi yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mudzagonjetsa mizinda yao yonse yamalinga ndi yabwinoyabwino ija. Mudzagwetsa mitengo yabwino yonse ndi kutseka akasupe onse a madzi, ndipo mudzaononga minda yao yonse yachonde, pakuponyamo miyala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:19
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza thumba ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.


Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu mu Afeki mpaka mudzawatha.


Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.


Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.


Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa