Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Elisa adati, “Pali Chauta Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamtumikira, pakadapanda kuti ndimamchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikadakusamalani ngakhale kukuyang'anani komwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:14
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pake, zedi, ndionekadi pamaso pake lero.


Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.


Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana.


M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.


Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mzinda walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, padziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko.


Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa