Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Tsono Elisa adafunsa mfumu Yoramu kuti “Inu kwanga kuno mwadzatani? Bwanji osapita kwa aneneri amene bambo wanu ndi mai wanu ankapemphako nzeru.” Koma Yoramu adati, “Iyai, pakuti Chauta ndiye amene waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.” Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:13
19 Mawu Ofanana  

Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?


Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.


Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.


Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo. Pamenepo mfumu ya Israele, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.


Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai;


Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?


Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?


Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.


Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa