Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 24:8 - Buku Lopatulika

8 Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Nehusita, mwana wa Elinati, wa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 24:8
8 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Yehoyakimu: Yekoniya mwana wake, Zedekiya mwana wake.


Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nachita choipa pamaso pa Yehova.


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiremo; m'menemo udzafa.


Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?


Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.


Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa