Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 24:7 - Buku Lopatulika

7 Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezenso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezanso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Ejipito sidatulukenso m'dziko lake, poti mfumu ya ku Babiloni inali italanda maiko onse a mfumu ya ku Ejipito kuchokera ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 24:7
10 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.


Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pamtsinje wa Yufurate mu Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.


Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pamtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.


Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwe kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lake.


ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja.


napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa