Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 24:4 - Buku Lopatulika

4 ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 ndiponso chifukwa cha magazi a anthu osachimwa amene iye adakhetsa. Manaseyu adadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osachimwa, ndipo Chauta sadamkhululukire ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 kuphatikizapo kukhetsa magazi a anthu osalakwa. Chifukwa iye anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kumukhululukira.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 24:4
20 Mawu Ofanana  

Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;


Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.


Koma Yehova sanakhululuke mkwiyo wake waukulu waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, chifukwa cha zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wake.


Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.


Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;


Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita mu Yerusalemu.


Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa;


Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.


Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.


Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;


Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukire.


Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.


Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera chilango, ndaika mwazi wake pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.


Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


kuti angakhetse mwazi wosachimwa pakati padziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, pangakhale mwazi pa inu.


Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa