Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 24:16 - Buku Lopatulika

16 Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono mfumu ya ku Babiloni idagwira ukapolo anthu otchuka onse okwanira 7,000, ndiponso anthu aluso pamodzi ndi amisiri osula 1,000. Onsewo anali amphamvu odziŵa kumenya nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 24:16
8 Mawu Ofanana  

Nachoka nao a mu Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko.


Koma mkulu wa olindirira anasiya osaukadi a m'dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi.


Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.


ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m'dzanja la Ababiloni.


anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,


Amenewa ndi anthu amene Nebukadinezara anatenga ndende: chaka chachisanu ndi chiwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;


ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m'dziko;


nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko aakulu, ndi maphiphi aatali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nkutenga nsonga ya mkungudza,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa