Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 24:10 - Buku Lopatulika

10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mzindawo misasa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nthaŵi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ku Yerusalemu, nazinga mzindawo ndi zithando zankhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Nthawi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ku Yerusalemu nazinga mzindawo ndi misasa ya nkhondo

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 24:10
8 Mawu Ofanana  

Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babiloni kumzinda, ataumangira misasa anyamata ake,


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita atate wake.


Ndipo mzindawo unazingidwa ndi timalinga mpaka chaka chakhumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya.


Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.


Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitilize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuluyo, limene liwazinga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa