2 Mafumu 24:1 - Buku Lopatulika1 Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pa nthaŵi ya Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo Yehoyakimu adakakamizidwa kutumikira Nebukadinezarayo zaka zitatu. Koma pambuyo pake Yehoyakimuyo adapandukira Nebukadinezara. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.