2 Mafumu 23:5 - Buku Lopatulika5 Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Yosiya adatulutsa ansembe a mafano amene mafumu a ku Yuda adaŵakhazika kuti azipereka nsembe ku akachisi ku mizinda ya m'dziko la Yuda ndi ku malo ozungulira Yerusalemu. Adatulutsanso amene ankapereka nsembe kwa Baala, kwa dzuŵa, kwa mwezi, kwa nyenyezi ndi kwa zinthu zonse zakuthambo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. Onani mutuwo |