2 Mafumu 23:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse m'Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tsono mfumu Yosiya adalamula Hilikiya, wansembe wamkulu, ndiponso ansembe othandiza ndi alonda apakhomo, kuti achotse m'Nyumba ya Mulungu zinthu zonse zopembedzera Baala, fano la Asera ndiponso mafano a zinthu zakuthambo. Zonsezo adazitenthera kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Kidroni, ndipo phulusa lake adapita nalo ku Betele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli. Onani mutuwo |