2 Mafumu 23:3 - Buku Lopatulika3 Niima mfumu pachiunda, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Niima mfumu pachiunda, nichita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Kenaka mfumuyo idaimirira pa nsanja yake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndiponso ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano chimenechi monga momwe adalembedwera m'bukulo. Tsono anthu onse nawonso adavomera kutsata chipanganocho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli. Onani mutuwo |
napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.