Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 23:11 - Buku Lopatulika

11 Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adachotsanso akavalo amene mafumu a ku Yuda adaaŵapereka ngati nsembe kwa dzuŵa. Akavalo amenewo ankaŵasunga pa bwalo la Nyumba ya Mulungu pafupi ndi chipata choloŵera m'Nyumbamo, ndiponso chipinda cha Natani Meleki, mkulu wosunga nyumbayo. Kenaka adatentha magaleta opembedzera dzuŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 23:11
8 Mawu Ofanana  

Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.


Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara.


Anachotsanso m'mizinda yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake.


Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.


ngati ndalambira dzuwa lilikuwala, kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;


Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.


Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa