Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono Hilikiya, mkulu wa nsembe uja, adauza Safani, mlembi uja, kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo Hilikiya adapereka bukulo kwa Safani, iye naliŵerenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:8
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova.


Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang'ono ndi aakulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.


Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa