Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:7 - Buku Lopatulika

7 Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma anthu amene apatsidwe ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo asaŵafunse kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti ndi anthu okhulupirika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.


kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.


Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.


ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.


Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri; koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.


Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.


Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.


Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa