Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:5 - Buku Lopatulika

5 ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova; iwo azipereke kwa ogwira ntchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 iwo azipereke kwa ogwira ntchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndalama zimenezo azipereke kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo azipereke kwa antchito aja okonza Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova,

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:5
8 Mawu Ofanana  

Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka.


kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.


Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.


Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa