Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 22:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono Safani adauza mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsira buku.” Ndipo Safani adaliŵerenga bukulo pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 22:10
17 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m'buku la chilamulo, inang'amba zovala zake.


Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova.


Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.


Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;


Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


Ndipo Mikaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu.


Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenga m'makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m'makutu ao.


Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kutuluka nao m'chipinda cha Elisama mlembi. Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akulu onse amene anaima pambali pa mfumu.


koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene atuluka m'mizinda yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa