1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
1 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adadaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
1 Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati.
Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.
Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.