Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 21:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono sindidzalola kuti Aisraele adzachotsedwe m'dziko lao limene ndidapatsa makolo ao, malinga kuti iwowo azisamala kuchita zinthu zonse motsata Malamulo amene ndaŵalamula, ndiponso motsata Malamulo amene Mose mtumiki wanga adaŵalamula.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 21:8
16 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja,


Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;


ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,


koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa