Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 21:5 - Buku Lopatulika

5 Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Manase yemweyo adamangira zinthu zakuthambo maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova, Manase anamangamo maguwa opembedzerapo zinthu zamlengalenga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 21:5
17 Mawu Ofanana  

Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.


Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.


Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.


Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.


Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.


Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.


Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu, nawataya kunja kwa mzinda.


Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.


Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.


Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m'bwalo lam'kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;


Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa chipata cha kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;


Ndi nsanamira zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.


Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.


Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.


Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.


Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.


Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa