Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 21:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Manaseyo adamanganso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaononga ku mapiri. Adamangira Baala maguwa, napanga mafano monga m'mene ankachitira Ahabu mfumu ya Aisraele. Ndipo ankapembedza zinthu zakuthambo namazitumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 21:3
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.


Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?


Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.


Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu.


Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?


Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.


ngati ndalambira dzuwa lilikuwala, kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;


Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;


Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Musazike kwa inu nokha mzati wa Ashera, wa mtengo uliwonse, pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.


Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake,


nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;


kuti angakuphunzitseni kuchita monga mwa zonyansa zao zonse, amazichitira milungu yao; ndipo mungachimwire Yehova Mulungu wanu.


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa