Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 21:22 - Buku Lopatulika

22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m'njira ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m'njira ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Adakana Chauta, Mulungu wa makolo ake, ndipo sadamvere malamulo ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Iyeyo anasiya Yehova Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 21:22
9 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wake, natumikira mafano anawatumikira atate wake, nawagwadira;


popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso.


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.


Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.


Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.


Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.


Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa