Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 21:1 - Buku Lopatulika

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mai wake anali Hepeziba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Manase anakhala mfumu ali ndi zaka khumi ndi ziwiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 55. Amayi ake anali Hefiziba.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 21:1
9 Mawu Ofanana  

Nagona Hezekiya ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Manase mwana wake.


Ahazi mwana wake, Hezekiya mwana wake, Manase mwana wake,


Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala mu Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.


Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.


Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.


Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita mu Yerusalemu.


Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.


ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa