Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mzinda uno m'dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mzinda uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mudzi uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya. Mzindawu ndidzautchinjiriza chifukwa cha ulemu wanga ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:6
7 Mawu Ofanana  

Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.


Nati Yesaya, Tenga nchinchi yankhuyu. Naitenga, naiika pafundo, nachira iye.


Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.


Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova.


Chifukwa chake atero Ambuye, Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito.


Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.


nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa