Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:14 - Buku Lopatulika

14 Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya, namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:14
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena mu ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.


Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.


Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.


Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.


Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.


a ku Babiloni, ndi Ababiloni, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasiriya onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.


Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.


Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa