Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena mu ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo, ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:13
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikenso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni.


Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera.


Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.


Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndi mure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.


Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.


Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.


Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu.


Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.


Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.


Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.


Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa