Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:12 - Buku Lopatulika

12 Nthawi ija Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babiloni anatumiza makalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Nthawi ija Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babiloni anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pa nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso, kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.


Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.


Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.


Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.


Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.


Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.


Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.


Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.


pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa