Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 20:10 - Buku Lopatulika

10 Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Hezekiyayo adayankha kuti, “Nchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, koma kuti chithunzithunzicho chibwerere m'mbuyo makwerero khumi, apo ndiponi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 20:10
9 Mawu Ofanana  

Nati iye, Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ai.


Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.


Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?


Ndipo ichi chidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amowabu m'dzanja lanu.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.


Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.


Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa