Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m'njiramo, munatuluka anyamata aang'ono m'mzindamo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m'njiramo, munatuluka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Kuchokera kumeneko Elisa adapita ku Betele. Ndipo pamene anali pa njira, anyamata ena amumzindamo adatuluka nayamba kumseka kuti, “Choka apa, chidazi! Choka apa, chidazi!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:23
34 Mawu Ofanana  

Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.


Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.


Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele.


Chotero madzi anachiritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.


koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.


Angakhale ana aang'ono andipeputsa, ndikanyamuka, andinena;


Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.


Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.


Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.


Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe, ananding'amba osaleka.


Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.


Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.


Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.


Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe.


Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.


Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa.


Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.


Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.


Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.


Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.


Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.


kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa