Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono Elisa adapita ku kasupe wa madzi, nathiramo mchere m'kasupemo, nati, “Chauta akunena kuti, ‘Madzi ameneŵa ndaŵakonza. Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo, m'madzi ameneŵa simudzakhala chinthu chopha anthu kapena choletsa nthaka kubereka.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:21
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye.


Chotero madzi anachiritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.


Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe chowawa.


Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.


Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.


Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.


Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.


Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso,


ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa