2 Mafumu 2:20 - Buku Lopatulika20 Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Apo Elisa adati, “Patseni mbale yatsopano, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo adabweradi ndi mchere m'mbale. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye. Onani mutuwo |
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.