Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo amuna amumzinda anati kwa Elisa, Taonani, mumzinda muno m'mwabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo amuna akumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Tsiku lina anthu amumzinda adauza Elisa kuti, “Onani, mzinda wathuwu ngwabwino kwambiri, zonse zili bwino monga mukuwoneramu, koma madzi okha ngoipa, ndipo nthaka yake njosabereka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:19
16 Mawu Ofanana  

M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.


Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?


Ndipo Obadiya ali m'njira taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?


Nabwerera kwa iye ali chikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanene nanu, Musamuka?


Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye.


Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a pa Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara.


M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.


Apatseni, Yehova; mudzapatsa chiyani? Muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.


Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.


Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.


Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.


Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.


Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa