2 Mafumu 2:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya paphiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Ndipo iwo adamuuza kuti, “Taonani tsono, ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Chonde mulole kuti anyamuke akamufunefune mbuyanu Eliya. Mwina mwake mzimu wa Chauta wamtenga nkukamponya kuphiri kwina kapena ku chigwa.” Elisayo adati, “Iyai musaŵatume.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.” Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.” Onani mutuwo |