Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:13 - Buku Lopatulika

13 Pamenepo anatola chofunda chake cha Eliya chidamtayikiracho, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pamenepo anatola chofunda chake cha Eliya chidamtayikiracho, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kenaka adatenga mwinjiro wa Eliya umene udaagwa, nabwerera nkukaima pa gombe la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:13
7 Mawu Ofanana  

Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.


Ndipo mfumu Solomoni anamanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere uli pafupi ndi Eloti, m'mphepete mwa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.


Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.


Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.


Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.


anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,


Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa