Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 19:8 - Buku Lopatulika

8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 19:8
10 Mawu Ofanana  

Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golide.


Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,


Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.


Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala mu Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe.


Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye anapitirira kuchokera ku Makeda kunka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;


mfumu ya ku Yaramuti, imodzi; mfumu ya ku Lakisi, imodzi;


mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;


Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;


Libina ndi Eteri ndi Asani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa