Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 19:7 - Buku Lopatulika

7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 19:7
17 Mawu Ofanana  

Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.


Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m'mzinda muno, ati Yehova.


Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.


Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.


M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.


Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.


Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala mu Lebi-kamai, mphepo yoononga.


Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.


Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa