Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 19:11 - Buku Lopatulika

11 Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka?

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 19:11
9 Mawu Ofanana  

Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?


Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asiriya.


Kodi milungu ya amitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?


Analemberanso makalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditse anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m'dzanja mwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa