Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 18:8 - Buku Lopatulika

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Adakantha Afilisti mpaka ku Gaza ndi ku dera lake lonse. Adaononga mudzi uliwonse ndi mzinda uliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye anakantha Afilisti kuyambira ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa. Anakafika mpaka ku Gaza ndi ku malire ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 18:8
9 Mawu Ofanana  

Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera.


Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'mizinda mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumzinda walinga komwe.


Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.


Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.


Afilisti omwe adagwa m'mizinda ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi midzi yake, ndi Timna ndi midzi yake, ndi Gimizo ndi midzi yake; nakhala iwo komweko.


Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.


ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.


Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao).


Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa