Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 18:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iyeyo ankakangamira kwa Chauta. Sadaleke kutsata Chauta, koma ankasunga malamulo amene Iye adapatsa Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye anakangamira Yehova ndipo sanamusiye koma anasunga malamulo amene Yehova anapatsa Mose.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 18:6
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.


Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israele amene adawaika.


Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.


Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.


limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;


Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.


Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.


Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,


Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.


koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munachita mpaka lero lino.


Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa